🌰 SABLE FARMING COMPANY LIMITED
Telephone: 0212 388 388 | E-mail: sable@sablefarming.com
P.O. Box 51199, Limbe, Malawi
KULEMBA ANTCHITO A NYENGO YA MACADAMIA FACTORY
Kampani ya Sable Farming – Mapanga ikufuna kulemba a ntchito a nyengo (seasonal workers) kuti azigwira ntchito ku Macadamia Factory.
Zofunikira:
- Anthu onse omwe ali ndi chiidwi atha kulembela ntchito imeneyi.
- Ayenera kukhala nzika ya Malawi ndipo kukhala ndi zaka zopitirira 18.
- Ayenera kukhala ndi National Identity Card ndipo osakhala ndi mbiri ya milandu.
- Kudziwa kusankha ndi kugwiritsa ntchito Macadamia kudzakhala mwayi wowonjezera.
- Anthu ochepa okha (osankhidwa) ndi amene adzaitanidwe ku mayesero (interviews).
- Tsiku lomaliza kulandira kalata zofunsira ntchito ndi Loweruka, 8 Novembala 2025.
Malangizo Ofunika:
Sable Farming Company Ltd ndi kampani yomwe imatsatira mfundo za mpata wofanana kwa onse (Equal Opportunity Employer) ndipo ili ndi ndondomeko ya Zero Tolerance pa nkhanza zogonana, kuzunza ogwira ntchito, ndi tsankho lililonse kuntchito.
Ntchito ku Sable Farming ndiyopanda kulipira chilichonse. Ngati munthu aliyense akukupemphani ndalama kapena mphatso kuti akuthandizeni mu ntchito imeneyi, munenezeni nthawi yomweyo pogwiritsa ntchito manambala omwe ali pama board a pakhomo (gate notice boards).
Ine Wanu,
Peter Stephano
Human Resources Manager
For: Sable Farming Co. Ltd
Cc: GM, DGMs, OM1, FC, CA
Please address all correspondence to the General Manager.
📢 Hashtags: #SableFarming #MalawiJobs #MacadamiaFactory #SeasonalJobs #EqualOpportunityEmployer #AgricultureJobs #FarmingOpportunities #JobAlertMalawi #WorkInMalawi #FarmEmployment
Comments
Post a Comment